Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 10:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo ine Danieli ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaona masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukuru, nathawa kubisala.

8. Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya akuruwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika cibvundi mwa ine, wosakhalanso ndi mphamvu ine.

9. Ndipo ndinamva kunena kwa mau ace, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ace ndinagwidwa ndi tulo tatikuru pankhope panga, nkhope yanga pansi.

10. Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.

11. Nati kwa ine, Danieli, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndirikunena ndi iwe, nukhale ciriri; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera.

12. Pamenepo anati kwa ine, Usaope Danieli; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzicepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako,

13. Koma kalonga wa ufumu wa Perisiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.

Werengani mutu wathunthu Danieli 10