Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 9:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwaiwosadzapulumukadi.

2. Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.

3. Angakhale abisala pamwamba pa Karimeli, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.

4. Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwacitira coipa, si cokoma ai.

5. Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzacita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Aigupto;

6. ndiye amene amanga zipinda zace zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lace pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lace ndiye Yehova.

7. Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israyeli? ati Yehova. Sindinakweza Israyeli ndine, kumturutsa m'dziko la Aigupto, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?

8. Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wocimwawo, ndipo ndidzauononga kuucotsa pa dziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova.

9. Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israyeli mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'licero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse.

10. Ocimwa onse a anthu anga adzafa ndi lupanga, ndiwo amene akuti, Coipa sicidzatipeza, kapena kutidulira.

11. Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zace; ndipo ndidzautsa zogumuka zace, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;

12. kuti alandire otsala a Edomu akhale colowa cao, ndi amitundu onse akuchedwa dzina langa, ati Yehova wakucita izi.

Werengani mutu wathunthu Amosi 9