Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwaiwosadzapulumukadi.