Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 9:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yace pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.

7. Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.

8. Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya garu wakufa monga ine.

9. Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Sauli, ninena naye, Za Sauli zonse ndi za nyumba yace yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.

10. Ndipo uzimlimira munda wace, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zace kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.

11. Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzacita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.

12. Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lace ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 9