Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.