Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 9:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Sauli, kuti ndimcitire cifundo cifukwa ca Jonatani?

2. Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Sauli dzina lace Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu ame.

3. Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Sauli kuti ndimuonetsere cifundo ca Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Jonatani wopunduka mapazi ace.

4. Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri, mwana vya Amiyeli ku Lodebara.

5. Pamenepo Davide anatumiza anthu nakatenga iye ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyeli ku Lodebara.

6. Ndipo Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yace pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.

7. Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.

8. Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya garu wakufa monga ine.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 9