Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 8:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

6. Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko, Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kuli konse anamukako.

7. Ndipo Davide anatenga zikopa zagolidi zinali ndi anyamata a Hadadezeri, nabwera nazo ku Yerusalemu.

8. Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezeri, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.

9. Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezeri,

10. Toi anatumiza mwana wace Joramu kwa mfumu Davide, kuti akamlankhule iye, ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezeri ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezeri ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Joramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zotengera zamkuwa.

11. Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa;

12. za Aaramu, za Amoabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleki, ndi zofunkha za Hadadezeri, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.

13. Ndipo Davide anamveketsa dzina lace pamene anabwera uko adakantha Aaramu m'cigwa ca mcere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.

14. Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.

15. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, Davide naweruza ndi cilungamo mirandu ya anthu onse.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 8