Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 7:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwace, atampumulitsa Yehova pa adani ace onse omzungulira,

2. mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndirikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu liri m'kati mwa nsaru zocinga.

3. Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani mucite conse ciri mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu,

4. Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti,

5. Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

6. pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinaturutsa ana a Israyeli ku Aigupto kufikira lero lomwe, kama ndinayenda m'cihema ndi m'nyumba wamba.

7. M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israyeli kodi ndinanena ndi pfuko limodzi la Aisrayeli, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisrayeli, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?

8. Cifukwa cace tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakucotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israyeli,

9. Ndipo ndinali nawe kuli konse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akuru ali pa dziko lapansi,

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 7