Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 6:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pambuyo pace Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israyeli, anthu zikwi makumiatatu.

2. Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nacokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amachula nalo Dzinalo Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.

3. Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa gareta watsopano, ataliturutsa m'nyumba ya Abinadabu, iri pacitunda, ndipo Uza ndi Ahio ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa gareta watsopanoyo.

4. Poturuka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu iri pacitunda, Ahio anatsogolera likasalo.

5. Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israyeli anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoyimbira za mitundu mitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi masece, ndi nsanje.

6. Ndipo pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lace, nacirikiza likasa la Mulungu; cifukwa ng'ombe zikadapulumuka.

7. Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, cifukwa ca kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.

8. Ndipo kudaipira Davide, cifukwa Yehova anacita cipasulo ndi Uza; nacha-malowo Cipasulo ca Uza, kufikira lero lino.

9. Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 6