Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 3:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mulungu alange Abineri, naonjezepo, ndikapanda kumcitira Davide monga Yehova anamlumbirira;

10. kucotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazika mpando wadfumu wa Davide pa Israyeli ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.

11. Ndipo iye sanakhoza kuyankha Abineri mau amodzi cifukwa ca kumuopa iye.

12. Ndipo Abineri anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisrayeli onse atsate inu.

13. Nati iye, Cabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira cinthu cimodzi, ndico kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Sauli, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.

14. Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Sauli, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.

15. Pomwepo Isiboseti anatumiza namcotsera kwa mwamuna wace, kwa Palitieli mwana wa Laisi.

16. Ndipo mwamuna waceyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Baburimu. Pomwepo Abineri ananena naye, Coka, bwerera; ndipo anabwerera.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 3