Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 23:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lace linalema, ndi dzanja lace lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwace kukafunkha kokha.

11. Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Mharario Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12. Koma iyeyoanaima pakati pa mundawo, naucinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anacititsa cipulumutso cacikuru.

13. Ndipo atatu a mwamakumi atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti Gnamanga zithando m'cigwa ca Refaimu.

14. Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu.

15. Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! wina akadandipatsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri pacipatapo!

16. Ndipongwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'citsime ca ku Betelehemu, ca pa cipataco, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafuna kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17. Nati, Ndisacite ici ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa ana pitawa ndi kutaya moyo wao? Cifukwa cace iye anakana kumwa. Izi anazicita ngwazi zitatuzi.

18. Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19. Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? cifukwa cace anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba.

20. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabzeli amene anacita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Moabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya cipale cofewa;

21. ndipo anapha M-aigupto munthu wokongola, M-aigupto anali nao mkondo m'dzanja lace; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 23