Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 21:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. mutipatse ana ace amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapacika kwa Yehova m'Gibeya wa Sauli, wosankhika wa Yehova, Mfumu niti, Ndidzawapereka.

7. Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, cifukwa ca lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Jonatani mwana wa Sauli.

8. Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Sauli, ndiwo Arimoni ndi, Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, amene iye anambalira Adriyeli mwana wa Barizilai Mmeholati;

9. niwapereka m'manja a Agibeoni, iwo nawapacika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kuceka barele.

10. Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga ciguduli, nadziyalira ici pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ocokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zirombo za kuthengo usiku.

11. Ndipo anauza Davide cimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Sauli anacita.

12. Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;

13. nacotsa kumeneko mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapacikidwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 21