Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 21:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anauza Davide cimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Sauli anacita.

12. Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;

13. nacotsa kumeneko mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapacikidwa.

14. Naika mafupa a Sauli ndi Jonatani mwana wace ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wace; nacita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pace Mulungu anapembedzeka za dzikolo.

15. Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisrayeli; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ace pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide.

16. Ndipo Isibenobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wace kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anabvala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

17. Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfliistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzaturuka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israyeli.

18. Ndipo kunali citapita ici, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 21