Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 21:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo m'masiku a Davide munali odala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndico cifukwa ca Sauli ndi nyumba yace yamwazi, popeza iye anawapha Agibeoni.

2. Ndipo mfumu inaitana Agibeoni, ninena nao (koma Agibeoni sanali a ana a Israyeli, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israyeli anawalumbirira kwa iwo, koma Sauli anafuna kuwapha mwa cangu cace ca kwa ana a Israyeli ndi a Yuda).

3. Ndipo Davide ananena ndi Agibeoni, Ndidzakucitirani ciani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi ciani kuti mukadalitse colowa ca Yehova?

4. Ndipo Agibeoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golidi wa Sauli kapena nyumba yace; ndiponso sitifuna kupha munthu ali yense wa m'Israyeli. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakucitirani.

5. Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife cotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israyeli,

6. mutipatse ana ace amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapacika kwa Yehova m'Gibeya wa Sauli, wosankhika wa Yehova, Mfumu niti, Ndidzawapereka.

7. Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, cifukwa ca lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Jonatani mwana wa Sauli.

8. Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Sauli, ndiwo Arimoni ndi, Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Sauli, amene iye anambalira Adriyeli mwana wa Barizilai Mmeholati;

9. niwapereka m'manja a Agibeoni, iwo nawapacika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kuceka barele.

10. Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga ciguduli, nadziyalira ici pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ocokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zirombo za kuthengo usiku.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 21