Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 20:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mudzimo anapfuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yoabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndgankhule nanu.

17. Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yoabu kodi? iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndirikumva.

18. Ndipo iye analankhula, nati, Kale adafunena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abeli; ndipo potero mrandu udafukutha.

19. Inendine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika m'Israyeli; inu mulikufuna kuononga mudzi ndi mai wa m'Israyeli; mudzamezerang colowa ca Yehova?

20. Ndipo Yoabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, cikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga.

21. Mranduwo soli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efraimu, dzina lace ndiye Seba mwana wa Bikri, anakweza dzanja lace pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzacoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yoabu, Onani tidzakuponyerani mutu wace kutumphitsa Gnga.

22. Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yace. Ndipo iwo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikri, nauponya kunja kwa Yoabu. Ndipo analiza Gpenga, nabalalika kucoka pamudzipo, munthu yense kumka ku hema wace. Ndipo Yoabu anabwerera kumka ku Yerusalemu kwa mfumu.

23. Ndipo Yoabu anali woyang'anira khamu lonse la Israyeli; ndi Benaya, mwana wa Jehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;

24. ndi Adoramu anayang'anira msonkho; ndi Jehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri;

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 20