Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 18:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera cilango adani ace.

20. Ndipo Yoabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, cifukwa mwana wa mfumu wafa.

21. Pamenepo Yoabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yoabu, nathamanga.

22. Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kaciwiri kwa Yoabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yoabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo?

23. Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange, iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kucigwa, napitirira Mkusi.

24. Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la cipata ca kulinga, natukula maso ace, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.

25. Pamenepo mlondayo anapfuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira.

26. Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakucipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, iyenso abwera ndi mau.

27. Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki, Ndipo mfumu inati, iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.

28. Ndipo Ahimaazi anapfuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yace pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.

29. Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yoabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringu piringu, koma sindinadziwa ngati kutani.

30. Ndipo mfumu inati, Pambuka nuime apa. Napambuka, naimapo.

31. Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera cilango lero onse akuukira inu.

32. Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukucitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.

33. Ndipo mfumuyo inagwidwa cisoni, nikwera ko cipinda cosanja pa cipataco, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 18