Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 17:20-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Jonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kumka ku Yerusalemu.

21. Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anaturuka m'citsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofeli anapangira zotere pa inu.

22. Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordano. Kutaca m'mawa sanasowa mmodzi wa iwo wosaoloka Yordano.

23. Ndipo Ahitofeli, pakuona kuti sautsata uphungu wace anamanga buru wace, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lace, nadzipacika, nafa, naikidwa m'manda a atate wace.

24. Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordano, iye ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye.

25. Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yoabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lace Itra M-israyeli, amene analowa kwa Abigayeli, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yoabu.

26. Ndipo Israyeli ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Gileadi.

27. Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyeli wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgileadi wa ku Rogelimu,

28. iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,

29. ndi uci ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kutiadye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'cipululumo.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 17