Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 16:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi cimeneci ndi cifundo cako ca pa bwenzi lako? unalekeranji kupita ndi bwenzi lako?

18. Husai nanena ndi Abisalomu, lai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israyeli, ine ndiri wace, ndipo ndidzakhala naye iyeyu.

19. Ndiponso ndidzatumikira yani? si pamaso pa mwana wace nanga? monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu,

20. Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofeli, Upangire cimene ukuti rikacite.

21. Ndipo Ahitofeli ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi ang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisrayeli onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba.

22. Comweco iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi ang'ono a atate wace pamaso pa Aisrayeli onse.

23. Ndipo uphungu wa Ahitofeli anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofeli unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu yemwe.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 16