Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 16:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao aburu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi ncinci zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo.

2. Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Aburuwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufoka m'cipululu akamweko.

3. Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israyeli idzandibwezera ufumu wa atate wanga.

4. Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse ziri zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 16