Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 15:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Comweco ananyamuka, nanka ku Hebroni.

10. Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israyeli, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.

11. Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.

12. Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofeli Mgiloni, mphungu wa Davide, ku mudzi wace ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo ciwembuco cinali colimba; pakuti anthu anacurukacurukabe kwa Abisalomu.

13. Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israyeli itsata Abisalomu.

14. Ndipo Davide ananena nao anyamata ace onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kucoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa.

15. Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 15