Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 14:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti Iyo, Nena.

13. Ndipo mkaziyo anati, Cifukwa ninjinso munalingalira cinthu cotere pa anthu a Mulungu? pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga woparamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wace.

14. Pakuti kufa tidzafa, ndipo tiri ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sacotsa moyo, koma alingalira ngra yakuti wotayikayo asakhale womtayikira iye.

15. Cifukwa cace tsono cakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndico kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzacita copempha mdzakazi wace.

16. Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wace m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kuticotsa ku colowa ca Mulungu.

17. Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.

18. Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 14