Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 13:9-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anatenga ciwaya natiturutsa pamaso pace; koma anakana kudya. Ndipo Amnoni anati, Anthu onse aturuke kundisiya ine. Naturuka onse, kumsiya.

10. Ndipo Amnoni anati kwa Tamara, Bwera naco cakudya kucipinda kuti ndikadye ca m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kucipinda kwa Amnoni mlongo wace.

11. Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.

12. Koma iye anamyankha nati, lai, mlongo wanga, usandicepetsa ine, pakuti cinthu cotere siciyenera kucitika m'Israyeli, usacita kupusa kumeneku.

13. Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israyeli. Cifukwa cace tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine.

14. Koma iye sadafuna kumvera mau ace, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkangamiza, nagona naye.

15. Atatero Amnoni anadana naye ndi cidani cacikuru kopambana; pakuti cidani cimene anamuda naco, cinali cacikuru koposa cikondi adamkonda naco. Ndipo Amnoni ananena naye, Nyamuka, coka.

16. Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti coipa ici cakuti ulikundipitikitsa ncacikuru coposa cina cija unandicitira ine. Kama anakana kumvera.

17. Pomwepo anaitana mnyamata wace amene anamtumikira, nati, Turutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze citseko atapita iye.

18. Ndipo iye anabvala cobvala ca mawanga mawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amabvala zotere. Ndipo mnyamata wace anamturutsa, napiringidza citseko atapita iye.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 13