Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 13:31-39 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zobvala zace nigona pansi, ndipo anyamata ace onse anaimirirapo ndi zobvala zao zong'ambika.

32. Ndipo Jonadabu mwana wa Simeya mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Amnoni yekha wafa, pakuti Ici cinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anacepetsa mlongo: wace Tamara.

33. Cifukwa cace tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi cinthuci, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Amnoni yekha wafa.

34. Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ace nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwace anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri.

35. Ndipo Jonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo.

36. Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ace analira ndi kulira kwakukuru ndithu.

37. Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihuri mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wace tsiku ndi tsiku.

38. Comweco anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu.

39. Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, cifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Amnoni.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 13