Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 13:21-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Koma pamene mfumu Davide anamva zonsezi, anakwiya ndithu.

22. Ndipo Abisalomu sanalankhula ndi Arononi cabwino kapena coipa, pakuti Abisalomu anamuda Amnoni, popeza adacepetsa mlongo wace Tamara.

23. Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali: nao osenga nkhosa zace ku Baalahazore pafupi pa Efraimu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu.

24. Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata, wanu ndiri nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu.

25. Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, lai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakucurukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.

26. Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Amnoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, iye apitirenji nawe?

27. Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Amnoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye.

28. Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ace, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Amnoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Amnoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, citani camuna.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 13