Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 12:8-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa cifukato cako, ndinakupatsanso nyumba ya Israyeli ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakucepera ndikadakuonjezera zina zakuti zakuti.

9. Cifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kucita cimene ciri coipa pamaso pace? Unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wace akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.

10. Cifukwa cace tsono lupanga silidzacoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Mhiti akhale mkazi wako.

11. Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzacotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa liri denene.

12. Pakuti iwe unacicita m'tseri; koma Ine ndidzacita cinthu ici pamaso pa Aisrayeli onse, dzuwa liri nde.

13. Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinacimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wacotsa chimo lanu, simudzafa.

14. Koma popeza pakucita ici munapatsa cifukwa cacikuru kwa adani a Yehova ca kucitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.

15. Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.

16. Cifukwa cace Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.

17. Ndipo akuru a m'nyumba yace ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.

18. Ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwang kuti mwana wafa; sadzadzicitira coipa nanga?

19. Koma pamene Davide anaona anyamata ace alikunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ace, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 12