Cifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kucita cimene ciri coipa pamaso pace? Unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wace akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.