Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 1:5-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwang kuti Sauli ndi Jonatani mwana wace anafa?

6. Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Giliboa, ndinaona, Sauli alikuyedzamira nthungo yace, ndi magareta ndi apakavalo anamyandikiza.

7. Ndipo iye pakuceukira m'mbuyo mwace anandiona, nanditana. Ndipo ndinayankha, Ndine.

8. Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine M-amaleki.

9. Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, cifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe.

10. M'mwemo ndinakhala pambali pace ndi kumtsiriza cifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wace, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pace, ndi cigwinjiri ca pa mkono wace, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga.

11. Pomwepo Davide anagwira zobvala zace nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye.

12. Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, cifukwa ca Sauli ndi mwana wace Jonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israyeli, cifukwa adagwa ndi lupanga.

13. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, M-amaleki.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 1