Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 36:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace.

6. Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babulo.

7. Nebukadinezara anatenganso zipangizo za nyumba ya Yehova kumka nazo ku Babulo, naziika m'kacisi wace ku Babulo.

8. Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

9. Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nacita coipa pamaso pa Yehova.

10. Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babulo, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.

11. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi,

12. nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace; sanadzicepetsa kwa Yeremiya mneneri wakunena zocokera pakamwa pa Yehova.

13. Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lace, nalimbitsa mtima wace kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli,

14. Ndiponso ansembe akulu onse ndi anthu anacurukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene ana patula m'Yerusalemu.

15. Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo, ndi dzanja la mithenga yace, nalawirira mamawa kuituma, cifukwa anamvera cifundo anthu ace, ndi pokhala pace;

16. koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ace, naseka aneneri ace, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ace, mpaka panalibe colanditsa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 36