Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 36:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anthu a m'dziko anatenga Yehoahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu m'Yerusalemu, m'malo mwa atate wace.

2. Yehoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu.

3. Ndipo mfumu ya Aigupto anamcotsera ufumu wace m'Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi a siliva, ndi talente limodzi la golidi.

4. Ndi mfumu ya Aigupto anamlonga Eliyakimu mng'ono wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lace likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehoahazi mkuru wace, namuka naye ku Aigupto.

5. Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace.

6. Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babulo.

7. Nebukadinezara anatenganso zipangizo za nyumba ya Yehova kumka nazo ku Babulo, naziika m'kacisi wace ku Babulo.

8. Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

9. Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nacita coipa pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 36