Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 35:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kucita Paskha, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.

17. Ndipo ana a Israyeli okhalako anacita Paskha nthawi yomweyo, ndi madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri.

18. Panalibe Paskha wocitika m'Israyeli wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samueli mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israyeli anacita Paskha wotere, ngati ameneyu anacita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisrayeli opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.

19. Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anacita Paskha amene.

20. Citatha ici conse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aigupto anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Firate; ndipo Yosiya anamturukira kuyambana naye.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 35