Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 34:12-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo amunawo anacita nchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yohati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena ali yense wa luso la zoyimbira,

13. Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira nchito ya utumiki uli wonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira.

14. Ndipo pakuturutsa ndarama zimene adalowa nazo ku nyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la cilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.

15. Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani.

16. Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzicita.

17. Nakhuthula ndarama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a anchito.

18. Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

19. Ndipo kunali, atamva mfumu mau a cilamulo, anang'amba zobvala zace.

20. Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

21. Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israyeli ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukuru; popeza makolo athu sanasunga mau a Yehova kucita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu.

22. Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasire wosunga zobvala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nanena naye mwakuti.

23. Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

24. Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo coipa, ndico matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda;

25. cifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.

26. Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kunena za mau udawamva,

27. popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ace otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzicepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zobvala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.

28. Taona, ndidzakusonkhanitsa ku makolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.

29. Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akulu akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 34