Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 33:5-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehoya.

6. Anapititsanso ana ace pamoto m'cigwa ca ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.

7. Ndipo anaika cifanizo cosema ca fanolo adacipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomo mwana wace, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israyeli ndidzaika dzina langa ku nthawi zonse;

8. ndipo sindidzasunthanso phazi la Israyeli ku dziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kucita zonse ndawalamulira, cilamulo conse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.

9. Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.

10. Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ace, koma sanasamalira.

11. Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asuri, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babulo.

12. Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wace, nadzicepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ace.

13. Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwace, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wace. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.

14. Citatha ici tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'cigwa, mpaka polowera pa cipata cansomba; nazinga Ofeli, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.

15. Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.

16. Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israyeli.

17. Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.

18. Macitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lace kwa Mulungu wace, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli, taonani, zalembedwa m'niacitidwe a mafumu a Israyeli.

19. Pemphero lace lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi chimo lace lonse, ndi kulakwa kwace, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzicepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.

20. Momwemo Manase anagona ndi makolo ace, namuika m'nyumba mwace mwace; ndi Amoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

21. Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 33