Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.