Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 31:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza.

12. Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkuru woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wace ndiye wotsatana naye.

13. Ndi Yeiyeli, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asaheli, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyeli, ndi Ismakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wace, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkuru wa ku nyumba ya Mulungu.

14. Ndipo Kore mwana wa Imna Mlevi, wa ku cipata ca kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulikitsa.

15. Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Minyamini, ndi Yesuwa; ndi Semaya, Amariya, ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akuru monga ang'ono;

16. pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa ali yense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa nchito yace pa tsiku lace, kukacita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;

17. ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao;

18. ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca ana ao ang'ono onse, akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m'kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika;

19. panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uli wonse, ochulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa cibadwidwe magawo ao.

20. Momwemo anacita Hezekiya mwa Yuda lonse nacita cokoma, ndi coyenera, ndi cokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wace.

21. Ndipo m'nchito iri yonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'cilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wace, anacita ndi mtima wace wonse, nalemerera nayo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 31