Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 25:8-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma ngati mumuka, citani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa.

9. Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israyeli? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani.

10. Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kucokera ku Efraimu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima.

11. Nalimbika mtima Amaziya, natsogolera anthu ace, namuka ku Cigwa ca Mcere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi.

12. Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, nawakankha pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo.

13. Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betihoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri.

14. Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yace, naigwadira, naifukizira,

15. Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu?

16. Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwacita ici ndi kusamvera kupangira kwanga.

17. Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yoasi mwana wa Yehoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani, tionane maso.

18. Ndi Yoasi mfumu ya Israyeli anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebano inapitapo, nipondereza mtungwi.

19. Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu.

20. Koma wosamvera Amaziya, pakuti nca Mulungu ici kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 25