Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 23:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma Yehoyada wansembe anaturuka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mturutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo ali yense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.

15. Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku cipata ca akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.

16. Ndipo Yehoyada anacita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.

17. Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.

18. Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, ndi kukondwera ndi kuyimbira, monga mwa cilangizo ca Davide.

19. Ndipo anaika odikira ku makomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kali konse asalowemo.

20. Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu ku nyumba ya Yehova; nalowera pa cipata ca kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.

21. Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mudzi munali cete, atamupha Ataliya ndi lupanga.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 23