Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 18:13-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Nati Mikaya, Pali Yehova, conena Mulungu wanga ndidzanena comweci.

14. Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Gileadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzacita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu.

15. Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane coonadi cokha cokha m'dzina la Yehova?

16. Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense ku nyumba yace mumtendere.

17. Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzani kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa?

18. Nati iye, Cifukwa cace tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lirikuima pa dzanja lace lamanja, ndi pa dzanja lace lamanzere.

19. Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israyeli ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Gileadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.

20. Ndipo unaturuka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi ciani?

21. Nuti uwu, Ndidzaturuka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; turuka, ukatero kumene.

22. Ndipo tsono taonani, Yehova analonga mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anu awa, nakunenetserani coipa Yehova.

23. Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandicokera bwanji kulankhula ndi iwe?

24. Nati Mikaya, Tapenya, udzaona tsiku lolowa iwe m'cipinda cam'kati kubisala.

25. Ndipo mfumu ya Israyeli inati, Mumtenge Mikaya, mukambweze kwa Amoni kazembe wa mudzi, ndi kwa Yoasi mwana wa mfumu;

26. nimuziti, Itero mfumu, Mumuike uyu m'kaidi, ndi kumdyetsa cakudya comsautsa, ndi kummwetsa madzi omsautsa, mpaka ndikabwera mumtendere.

27. Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananena mwa ine. Natiiye, Tamverani, anthu inu nonsenu.

28. Momwemo mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera kumka ku Ramoti Gileadi.

29. Ndi mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu bvalani zobvala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israyeli, namuka iwo kunkhondo.

30. Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magareta ace, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yekha.

31. Ndipo kunali, pamene akapitao a magareta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israyeli. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anapfuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapambukitsa amleke.

32. Ndipo kunali, pamene akapitao a magareta anaona kuti sanali mfumu ya Israyeli anabwerera osamtsatanso.

33. Ndipo munthu anaponya mubvi wace ciponyeponye, namlasa pakati pa maluma a maraya ace acitsulo. Potero anati kwa woyendetsa garetayo, Tembenuza dzanja lako, nundicotse ku khamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 18