Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 12:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Anakwera ndi magareta cikwi cimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kuturuka m'Aigupto ngosawerengeka, Alubi, Asuki, ndi Akusi.

4. Ndipo analanda midzi yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu.

5. Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehabiamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu cifukwa ca Sisaki, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, cifukwa cace Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisaki.

6. Pamenepo akalonga a Israyeli ndi mfumu anadzicepetsa, nati, Yehova ali wolungama.

7. Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzicepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzicepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa cipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisaki.

8. Koma adzakhala akapolo ace, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko.

9. Ndipo Sisaki mfumu ya Aigupto anakwerera Yerusalemu, nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; anazicotsa zonse; anacotsanso zikopa zagolidi adazipanga Solomo.

10. Ndipo Rehabiamu mfumu anapanga m'malo mwa izo zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.

11. Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku cipinda ca olindirira.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 12