Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 8:7-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno.

8. Niti mfumu kwa Hazaeli, Tenga caufulu m'dzanja lako, nukamkumike munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzacira kodi nthenda iyi?

9. Namuka Hazaeli kukakomana naye, napita naco caufulu, ndico ca zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamila makumi anai, nafika naima pamaso pace, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzacira nthenda iyi?

10. Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzacira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.

11. Ndipo anamyang'ana cidwi, mpaka anacita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

12. Nati Hazaeli, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa coipa udzacitira ana a Israyeli; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.

13. Nati Hazaeli, Koma nanga kapolo wanu ali ciani, ndiye garu, kuti akacite cinthu cacikuru ici? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

14. Ndipo anacoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wace; ameneyo ananena naye, Anakuuza ciani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzacira ndithu.

15. Ndipo kunali m'mawa mwace, anatenga cimbwi, nacibviika m'madzi, naciphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaeli analowa ufumu m'malo mwace.

16. Ndipo caka cacisanu ca Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

17. Ndiye wa zaka makumi atatu ndi ciwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.

18. Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wace ndiye mwana wa Ahabu, nacita iye coipa pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 8