3. Koma polowera pa cipata panali amuna anai akhate, nanenana wma ndi mnzace, Tikhaliranji kuno mpaka kufa?
4. Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa.
5. Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pace pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo.
6. Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magareta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikuru; nanenana wina ndi mnzace, Taonani mfumu ya Israyeli watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aaigupto, atigwere.
7. Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi aburu ao, misasa iri cimangire; nathawa, apulumutse moyo wao.