Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 6:21-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Niti mfumu ya Israyeli kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe?

22. Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao.

23. Ndipo anwakonzera cakudya cambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzanso ku dziko la Israyeli.

24. Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse, nakwera, namangira misasa Samariya.

25. Koma m'Samariya munali njala yaikuru; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa buru unagulidwa ndalama zasiliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi ndalama zasiliva zisanu.

26. Ndipo popita mfumu ya Israyeli alikuyenda palinga, mkazi anampfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.

27. Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? kudwale kodi, kapena popondera mphesa

28. Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa.

29. Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wace ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wace.

30. Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zobvala zace alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali ciguduli m'kati pa thupi lace.

31. Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.

32. Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwace, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kucotsa mutu wanga? taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi citseko. Kodi mapazi a mbuye wace samveka dididi pambuyo pace?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 6