Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 4:34-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pace ndi pakamwa pace, maso ace ndi maso ace, zikhato zace ndi zikhato zace, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35. Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, cakuno kamodzi, cauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ace.

36. Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunemu uja, Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ace, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wace, naturuka.

38. Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pace; ndipo anati kwa mnyamata wace, Ika nkhali yaikuruyo, uphikire ana a aneneri.

39. Naturuka wina kukachera ndiwo kuthengo, napeza conga ngati mpesa, nacherapo zipuzi kudzaza m'pfunga mwace, nadza, nazicekera-cekera m'nkhali ya cakudya, popeza sanazidziwa.

40. Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali; pakudya cakudyaco, anapfuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanatha kudyako.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 4