Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 3:13-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Elisa anati kwamfumuya Israyeli, Ndiri ndi ciani ndi inu? mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israyeli inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.

14. Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pace, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.

15. Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, waothetemyayo ali ciyimbire, dzanja la Yehova linamgwera.

16. Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m'cigwa muno mukhale maenje okha okha.

17. Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma cigwaco cidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng'ombe zanu, ndi zoweta zanu.

18. Ndipo ici cidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amoabu m'dzanja lanu.

19. Ndipo mudzakantha midzi yonse ya matioga, ndi midzi yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.

20. Ndipo kunacitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.

21. Atamva tsono Amoabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'cuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.

22. Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amoabu madzi ali pandunji pao ali psyu ngati mwazi;

23. nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzace; ndipo tsopano, tiyeni Amoabu inu, tikafunkhe.

24. Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israyeli, Aisrayeli ananyamuka, nakantha Amoabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amoabu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 3