Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 3:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

2. Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.

3. Koma anakangamira zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene anacimwitsa nazo Israyeli, osalekana nazo.

4. Ndipo Mesa mfumu ya Moabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.

5. Kama kunacitika, atafa Ahabu mfumu ya Moabu anapandukana ndi mfumu ya Israyeli.

6. Ndipo mfumu Yehoramu anaturuka m'Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisrayeli onse.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 3