Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 24:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. ndipo Yoyakini mfumu ya Yuda anaturukira kwa mfumu ya Babulo, iye ndi mace, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi adindo ace; mfumu ya Babulo nimtenga caka cacisanu ndi citatu ca ufumu wace.

13. Naturutsa kucotsa komweko cuma conse ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolidi adazipanga Solomo mfumu ya Israyeli m'Kacisi wa Yehova, monga Yehova adanena.

14. Nacoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsala ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okha okha a m'dziko.

15. Nacoka naye Yoyakini kumka naye ku Babulo, ndi mace wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ace, ndi omveka a m'dziko; anacoka nao andende ku Yerusalemu kumka nao ku Babulo.

16. Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula cikwi cimodzi, onsewo acamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babulo anadza nao andende ku Babulo.

17. Ndipo mfumu ya Babulo analonga Mataniya mbale wa atate wace akhale mfumu m'malo mwace, nasanduliza dzina lace likhale Zedekiya.

18. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

19. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adacita Yoyakimu.

20. Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pace; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 24