Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 24:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku ace Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwerako, Yoyakimu nagwira mwendo wace zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.

2. Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Akasidi, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amoabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova: adawanena ndi dzanja la atumiki ace aneneriwo.

3. Zedi ici cinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwacotsa pamaso pace, cifukwa ca zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazicita;

4. ndiponso cifukwa ca mwazi wosacimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosacimwa; ndipo Yehova sanafuna kukhululukira.

5. Macitidwe ena tsono a Yoyakimu, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

6. Nagona Yoyakimu ndi makolo ace, ndipo Yoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

7. Koma mfumu ya Aigupto sinabwerezanso kuturuka m'dziko lace, pakuti mfumu ya Babulo idalanda kuyambira ku mtsinje wa Aigupto kufikira ku mtsinje Firate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aigupto.

8. Yoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la mace ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.

9. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adacita atate wace.

10. Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa.

11. Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babulo kumudzi, ataumangira misasa anyamata ace,

12. ndipo Yoyakini mfumu ya Yuda anaturukira kwa mfumu ya Babulo, iye ndi mace, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi adindo ace; mfumu ya Babulo nimtenga caka cacisanu ndi citatu ca ufumu wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 24