Koma mfumu ya Aigupto sinabwerezanso kuturuka m'dziko lace, pakuti mfumu ya Babulo idalanda kuyambira ku mtsinje wa Aigupto kufikira ku mtsinje Firate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aigupto.