Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 22:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;

5. iwo azipereke kwa ogwira nchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

6. kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.

7. Koma sanawawerengera ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anacita mokhulupirika.

8. Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

9. Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova.

10. Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

11. Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m'buku la cilamulo, inang'amba zobvala zace.

12. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Alabori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

13. Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukuru; popeza atate athu sanamvera mau a buku ili, kucita monga mwa zonse zotilemberamo.

14. Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tlkiva, mwana wa Harasi, wosunga zobvala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nalankhula naye.

15. Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 22