Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 21:8-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo sindidzacotsanso mapazi a Israyeli m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; cokhaci asamalire kucita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa cilamulo conse anawalamulira Mose mtumiki wanga.

9. Koma sanamvera, nawalakwitsa Manase, nawacititsa coipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israyeli.

10. Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ace aneneri, ndi kuti,

11. Popeza Manase mfumu ya Yuda anacita zonyansa izi, pakuti zoipa zace zinaposa zonse adazicita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ace;

12. cifukwa cace atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda coipa, cakuti yense acimvera cidzamliritsa mwini khutu.

13. Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu cingwe coongolera ca Samariya, ndi cingwe colungamitsira ciriri ca nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuibvundikira.

14. Ndipo ndidzataya cotsala ca colowa canga, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo cakudya ndi cofunkha ca adani ao onse;

15. popeza anacita coipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga citurukire makolo ao m'Aigupto, mpaka lero lino.

16. Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.

17. Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

18. Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.

19. Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.

20. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo amacitira Manase atate wace.

21. Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wace, natumikira mafano anawatumikira atate wace, nawagwadira;

22. nasiya Yehova Mulungu wa makolo ace, sanayenda m'njira ya Yehova.

23. Ndipo anyamata ace a Amoni anamcitira ciwembu, napha mfumuyo m'nyumba yace yace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 21