Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 21:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hefisiba.

2. Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.

3. Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wace adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema cifanizo, monga anacita Ahabu mfumu ya Israyeli, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.

4. Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa.

5. Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.

6. Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.

7. Ndipo anaika cifanizo cosema cimene adacipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomo mwana wace kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israyeli ndidzaikamo dzina langa kosatha.

8. Ndipo sindidzacotsanso mapazi a Israyeli m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; cokhaci asamalire kucita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa cilamulo conse anawalamulira Mose mtumiki wanga.

9. Koma sanamvera, nawalakwitsa Manase, nawacititsa coipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israyeli.

10. Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ace aneneri, ndi kuti,

11. Popeza Manase mfumu ya Yuda anacita zonyansa izi, pakuti zoipa zace zinaposa zonse adazicita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ace;

12. cifukwa cace atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda coipa, cakuti yense acimvera cidzamliritsa mwini khutu.

13. Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu cingwe coongolera ca Samariya, ndi cingwe colungamitsira ciriri ca nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuibvundikira.

14. Ndipo ndidzataya cotsala ca colowa canga, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo cakudya ndi cofunkha ca adani ao onse;

15. popeza anacita coipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga citurukire makolo ao m'Aigupto, mpaka lero lino.

16. Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.

17. Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

18. Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 21